Genesis 47:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndalama zonse zitaŵathera anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani, Aejipito ambiri adabwera kwa Yosefe, namuuza kuti, “Tipatseniko chakudya! Musatilekerere kuti tife, chitanipo kanthu! Ndalama zathu zonse zatha!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, Aejipito onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? Zatsirizika ndalama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Igupto ndi Kanaani ndalama zitawathera, Aigupto onse anabwera kwa Yosefe nati, “Tipatseni chakudya. Nanga tiferenji pamaso panu? Ndalama zathu zatha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Aigupto ndi m'dziko la Kanani, Aaigupto onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife cakudya; tiferenji pamaso panu? zatsirizika ndalama.