Genesis 47:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adabwera ndi zoŵeta zao kwa Yosefe, nasinthitsa ndi chakudya zoŵeta zaozo, monga akavalo, nkhosa ndi mbuzi, ng'ombe ndi abulu. Chaka chimenecho Yosefe adaŵapatsa chakudya anthuwo mosinthana ndi zoŵeta zaozo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza nazo ng'ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo chakudya chosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi abulu; ndipo anawadyetsa iwo ndi chakudya chosinthana ndi zoweta zao zonse chaka chimenecho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthu anabwera ndi ziweto zawo monga akavalo, nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi abulu ndipo Yosefe anawapatsa zakudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza nazo ng'ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo cakudya cosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu; ndipo anawadyetsa iwo ndi cakudya cosinthana ndi zoweta zao zonse caka cimeneco.