Genesis 47:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chitatha chaka chimenecho, anthuwo adapitanso kwa Yosefe namuuza kuti, “Bwana, ife sitingakubisireni kuti ndalama zathu pamodzi ndi zoŵeta zathu zomwe, zatithera. Palibe chilichonse chotsala choti tingathe kukupatsani, tingodzipereka ifeyo ndi minda yathuyi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chitatha chaka chimenecho, anadza kwa iye chaka chachiwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe nza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chitatha chaka chimenecho, anthu anapitanso kwa Yosefe chaka chinacho nati, “Ife sitingakubisireni mbuye wathu kuti ndalama zathu zatithera ndipo ziweto zathu zili ndi inu, palibenso choti nʼkukupatsani mbuye wathu kupatula matupi athu ndi dziko lathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Citatha caka cimeneco, anadza kwa iye caka caciwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe oza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu;