Genesis 47:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musatilekerere kuti tife m'dziko mwathu, inu mukuwona. Mutipatseko chakudya, ndipo tidzigulitsa ifeyo ndi minda yathu yomwe. Tidzakhala akapolo a Farao, iye adzatenga minda yathu kuti ikhale yake. Mutipatseko mbeu kuti tisafe ndi njala, kutinso minda yathu isakhale masala.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tiferenji ife ndi dziko lathu inu mukuona? Mutipatse chakudya ndipo tidzigulitsa ife ndi minda yathu yomwe. Ife tidzakhala akapolo a Farao. Tipatseni mbewuzo kuti tikhale ndi moyo tisafe ndipo dziko lisachite bwinja.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? mutigule ife ndi dziko lathu ndi cakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.