Genesis 47:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yosefe adagulira Farao dziko lonse la Ejipito. Mwejipito aliyense adagulitsa minda yake chifukwa njalayo inali itafika poipa kwambiri. Motero dziko lonse lidasanduka la Farao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Ejipito, chifukwa Aejipito anagulitsa yense munda wake, chifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yosefe anamugulira Farao dziko lonse la Igupto. Aliyense mu Igupto anagulitsa munda wake chifukwa njala inakula kwambiri. Dziko lonse linasanduka la Farao,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Aigupto, cifukwa Aaigupto anagulitsa yense munda wace, cifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao.