Genesis 47:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko limene sadagule ndi la ansembe lokha. Iwowo sadagulitse dziko lao, popeza kuti Farao ankaŵapatsa chakudya choti azidya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma dziko la ansembe lokha sanagule, chifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; chifukwa chake sanagulitse dziko lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe, sanagule minda ya ansembe chifukwa Farao ankawapatsa thandizo lokwanira. Nʼchifukwa chake sanagulitse minda yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma dziko la ansembe lokha sanagule, cifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; cifukwa cace sanagulitsa dziko lao.