Genesis 47:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi yokolola mudzapereka kwa Farao chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse pa zokolola zanuzo, ndipo zina zonse zotsala zidzakhala zanu. Zina mudzasungire mbeu, koma zina mudzadye inuyo, mabanja anu ndi antchito anu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma podzakolola, mudzapereka gawo limodzi la magawo asanu aliwonse kwa Farao. Magawo anayi enawo adzakhala anu. Zina mudzasunge mbewu ndi zina mudzadye inuyo, mabanja anu ndi ana anu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za cakudya canu, ndi ca ana anu ndi mabanja anu.