Genesis 47:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Yosefe adapanga lamulo m'dziko lonse la Ejipito, kuti chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse pa zokolola chidzakhala cha Farao. Lamulo limeneli lilipobe mpaka lero lino. Koma maiko a ansembe okha sadaŵatenge kuti akhale a Farao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe analamulira lamulo la pa dziko la Ejipito kufikira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhala la Farao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yosefe anakhazikitsa lamulo limene lilipobe mpaka lero mʼdziko lonse la Igupto kuti limodzi la magawo asanu a zokolola ndi la Farao. Ndi minda ya ansembe yokha imene sinatengedwe kukhala ya Farao.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe analamulira lamulo la pa dziko la Aigupto kuukira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhala la Farao.