Genesis 47:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ali pafupi kumwalira, adaitana mwana wake Yosefe namuuza kuti, “Ngati ukundikondadi, undigwire m'kati mwa ntchafu zangazi, ulonjeze kuti udzandikomera mtima ndi kukhulupirika kwa ine, ndipo kuti mtembo wanga sudzauika ku Ejipito kuno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine m'Ejipito;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi itayandikira yoti Israeli amwalire, anayitanitsa mwana wake Yosefe nati kwa iye, “Ngati ukundikondadi monga abambo ako, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga ndipo ulonjeze kuti udzaonetsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwako kwa ine kuti sudzayika mtembo wanga kuno ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nthawi inayandikira kuti Israyeli adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wace wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ncafu yanga, nundicitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine m'Aigupto;