Genesis 47:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndifuna kukagona pamodzi ndi makolo anga. Mtembo wanga udzauchotse ku Ejipito kuno ukauike m'manda a makolo anga.” Yosefe adayankha kuti, “Ndidzachita monga momwe mwaneneramu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikagona pamodzi ndi makolo anga. Choncho ndikadzamwalira udzanditulutse mu Igupto muno ndipo ukayike mtembo wanga kumene anayikidwa makolo anga.” Yosefe anati, “Ndidzachita monga mwanenera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kuturuka m'dziko la Aigupto, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzacita monga mwanena.