Genesis 47:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko la Ejipito lili m'manja mwako. Ukhazike bambo wako pamodzi ndi abale ako m'dziko lachonde, akakhale ku Goseni. Ndipo ngati ena mwa iwo ndi akatswiri a zoŵeta, uŵapatse ukapitao woyang'anira zoŵeta zanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
dziko la Ejipito lili pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lonse la Igupto lili mʼdzanja lako. Uwakhazike abambo ako ndi abale ako mʼmalo achonde kwambiri. Akhale ku Goseni. Ndipo ngati ukudziwapo ena mwa iwo amene ali akatswiri pa kuweta ziweto, uwapatse udindo woyangʼanira ziweto zanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
dziko la Aigupto liri pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga.