Genesis 48:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yakobe adasemphanitsa manja. Motero adasanjika dzanja lake lamanja pamutu pa Efuremu amene anali wamng'ono, dzanja lamanzere adalisanjika pamutu pa Manase amene anali wamkulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pa mutu wa Efuremu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lake lamanzere pa mutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Israeli anapinganitsa mikono motero kuti anayika dzanja lake lamanja pamutu pa Efereimu ngakhale kuti iyeyo anali wamngʼono ndi dzanja lake lakumanzere analisanjika pamutu pa Manase ngakhale kuti iyeyu ndiye anali mwana woyamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Israyeli anatambalitsa dzanja lace lamanja, naliika pa mutu wa Efraimu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lace lamanzere pa mutu wa Manase anapingasitsa manja ace dala; cifukwa Manase anali woyamba.