Genesis 48:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo amene wandiwombola ku zoipa zonse, aŵadalitsenso! Podzera mwa anaŵa, dzina langa ndi maina a makolo anga Abrahamu ndi Isaki akhale omveka nthaŵi zonse! Adzakhale ndi ana ambiri iwoŵa, adzasanduke mtundu waukulu pa dziko lapansi!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse, ameneyo adalitse anyamata awa. Kudzera mwa iwowa dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka. Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulu pa dziko lapansi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa lichulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isake; iwo akule, nakhale khamu pakati pa dziko lapansi.