Genesis 48:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe ataona kuti bambo wake wasanjika dzanja lamanja pamutu pa Efuremu, adakhumudwa. Motero adatenga dzanja la bambo wake kulichotsa pamutu pa Efuremu, nalisanjika pamutu pa Manase.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pa mutu wa Efuremu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pa mutu wa Efuremu ndi kuliika pa mutu wa Manase.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe ataona kuti abambo ake ayika dzanja lamanja pa Efereimu, sanakondwere. Choncho anagwira dzanja la abambo ake kuti alichotse pamutu pa Efereimu ndi kuliyika pamutu pa Manase,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wace anaika dzanja lace lamanja pa mutu wa Efraimu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wace, kulicotsa pa mutu wa Efraimu ndi kuliika pa muta wa Manase.