Genesis 48:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma bambo wakeyo adakana nati, “Ndikudziŵa, mwana wanga, ndikudziŵa. Adzukulu a Manase adzakhalanso anthu otchuka, koma mng'ono wakeyu adzatchuka kupambana iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yaikulu ya anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma abambo ake anakana nati, “Ndikudziwa, mwana wanga, ndikudziwa. Adzukulu a iyeyunso adzakhala mtundu waukulu. Komabe mʼbale wake wamngʼonoyu adzakhala wamkulu kuposa iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yayikulu ya anthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anakana atate wace, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; Iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwace adzakhala wamkuru ndi iye, ndipo mbeu zace zidzakhala mitundu yambirimbiri.