Genesis 48:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adaŵadalitsa pa tsiku limenelo ndi mau akuti, “Aisraele adzatchula maina anu podalitsa. Adzanena kuti, ‘Mulungu akudalitseni inu monga Efuremu ndi Manase.’ ” Mwa njira imeneyi adaika Efuremu patsogolo pa Manase.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iye anawadalitsa tsiku limenelo nati, “Aisraeli adzagwiritsa ntchito dzina lanu podalitsa nadzati: Mulungu akudalitseni monga Efereimu ndi Manase.” Choncho anayika Efereimu patsogolo pa Manase.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israyeli adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efraimu ndi monga Manase; ndipo anaika Efraimu woyamba wa Manase.