Genesis 48:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adandiwuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri kotero kuti zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako kuti likhale lao mpaka muyaya.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakuchulukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao chikhalire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nati kwa ine, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri ndipo zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako zobwera pambuyo pako kuti likhale lawo mpaka muyaya.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakucurukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao cikhalire.