Genesis 48:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ana ako aŵiri, amene udabereka ku Ejipito kuno, ine ndisanabwere, amenewonso ndi anga. Efuremu ndi Manase adzakhala anga ndithu, monga momwe aliri Rubeni ndi Simeoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano ana ako amuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsopano ana ako aamuna awiri amene anabadwa ine ndisanabwere kuno adzakhala ana anga. Efereimu ndi Manase adzakhala anga monga mmene alili Rubeni ndi Simeoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano ana ako amuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Aigupto, ndisanadze kwa iwe ku Aigupto, ndiwo anga; Efraimu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.