Genesis 48:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndachita zimenezi chifukwa chakuti pamene ndinkabwerera kuchokera ku Mesopotamiya, mai wako Rakele adafera m'dziko la Kanani, mtunda wofika ku Efurata ukadalipo. Chisoni changa chinali chachikulu. Tsono ndidamuika komweko pa mseu wa ku Efurata ku Betelehemu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ndimabwerera kuchoka ku Parani, mwachisoni Rakele, amayi ako anamwalira mʼdziko la Kanaani, tikanali mʼnjira, mtunda wokafika ku Efurata ukanalipo. Ndipo ndinawayika kumeneko mʼmphepete mwa msewu wa ku Efurata” (amene ndi Betelehemu).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono ine, pamene ndinacokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efrati; ndipo ndidamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efrati (ndiwo Betelehemu).