Genesis 48:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe adayankha kuti “Ameneŵa ndi ana anga amene Mulungu adandipatsa ku Ejipito kuno.” Apo Yakobe adati, “Chonde abwere kuno anawo kuti ndiŵadalitse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe anati kwa abambo ake, “Awa ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kuno.” Ndipo Israeli anati, “Bwera nawo kuno kuti ndiwadalitse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.