Genesis 49:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bulu wake amamumangirira ku mtengo wamphesa, mwanawabulu ku mpesa wabwino. Zovala zake amazichapa mu vinyo, mu vinyo wofiira ngati magazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adamanga mwana wa kavalo wake pampesa, ndi mwana wa bulu wake pa mpesa wosankhika; natsuka malaya ake m'vinyo, ndi chofunda chake m'mwazi wa mphesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa, ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino. Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo; ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adamanga mwana wa kavalo wace pampesa, Ndi mwana wa buru wace pa mpesa wosankhika; Natsuka malaya ace m'vinyo, Ndi copfunda cace m'mwazi wa mphesa.