Genesis 49:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ataona kukoma kwa malo ousirapowo, ndi kukongola kwa dzikolo. Adaŵeramitsa msana kuti anyamule katundu wake, ndipo adasanduka womagwira ntchito yaukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino, ndi dziko kuti linali lokondweretsa; ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule, nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ataona ubwino wake wa pamalo pake popumira ndi kukongola kwa dziko lake, iye anaweramutsa msana kuti anyamule katundu wake ndipo anasanduka wogwira ntchito ya ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino, Ndi dziko kuti linali lokondweretsa; Ndipo anaweramitsa phewa lace kuti anyamule, Nakhala kapolo wakugwira nchito ya msonkho,