Genesis 49:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Yosefe ali ngati nthambi yobala zipatso, nthambi yobala zipatso pafupi ndi kasupe, nthambi yotambasuka pa khoma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yosefe ndi nthambi yobala, nthambi yobala pambali pa kasupe; nthambi zake ziyangayanga palinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yosefe ali ngati mtengo wobereka zipatso, mtengo wobereka zipatso pafupi ndi kasupe, nthambi zake zimayanga pa chipupa cha mwala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yosefe ndi nthambi yobala, Nthambi yobala pambali pa kasupe; Nthambi zace ziyangayanga palinga.