Genesis 49:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iyeyo uta wake sudagwedezeke, mikono yake idalimbika, ndi mphamvu za Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe, amene ali Mbusa ndi Thanthwe la Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma uta wake unakhala wamphamvu, ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa. Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo. (Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele,)
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma uta wake sunagwedezeke, ndi manja ake amphamvu aja analimbika, chifukwa cha mphamvu za Mulungu Wamphamvu wa Yakobo, chifukwa ali Mʼbusa ndi Thanthwe la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma uta wace unakhala wamphamvu, Ndi mikono ya manja ace inalimbitsidwa Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo. (Kucokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israyeli,)