Genesis 49:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi Mulungu wa atate ako amene amakuthandiza, ndi Mulungu Mphambe amene amakudalitsa. Amakudalitsa ndi mvula yochokera mu mlengalenga, ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka, ndipo adzakudalitsa pakukupatsa ana ambiri ndi ng'ombe zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza; chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa ndi mvula yochokera kumwamba, ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka, ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, Ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe Ndi madalitso a Kumwamba, Madalitso a madzi akuya akukhala pansi, Madalitso a mabere, ndi a mimba.