Genesis 49:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Madalitso a bambo wako ndi amphamvu kupambana madalitso a mapiri amuyaya, kupambananso zabwino za ku zitunda zamuyaya. Zimenezi zidzakhala pamutu pa Yosefe, pamphumi pa kalonga amene adampatula pakati pa abale ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Madalitso a atate wako apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga, aufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire. Adzakhala pa mutu wa Yosefe, ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa madalitso a mapiri akale oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona. Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe, pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Madalitso a atate wako Apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga, Kufikira ku malekezero a patari a mapiri a cikhalire; Adzakhala pa mutu wa Yosefe, Ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ace.