Genesis 49:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yakobe adaŵalamula ana akewo kuti, “Popeza kuti tsopano ndilikufa, mukandiike m'phanga limene lili m'munda wa Efuroni Muhiti, ku Makipera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanizidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga lili m'munda wa Efuroni Muhiti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanizidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga liri m'munda wa Efroni Mhiti,