Genesis 49:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Rubeni mwana wanga wachisamba, ndiwe nkhongono zanga, ndiwe mphatso yoyamba ya mphamvu zanga. Mwa ana anga onse, wopambana ndiwe pa ulemerero ndi mphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa; mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga, wopambana pa ulemerero ndi mphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi ciyambi ca mphamvu yanga; Ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.