Genesis 49:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lili kuvuma kwa Mamure m'dziko la Kanani. Abrahamu adaagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efuroni Muhiti, kuti pakhale manda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
m'phanga lili m'munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamure, m'dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pake:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ili ndi phanga la mʼmunda wa Makipela, pafupi ndi Mamre mʼdziko la Kanaani. Abrahamu anagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
m'phanga liri m'munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamre, m'dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efroni Mhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pace: