Genesis 49:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine sindidzakhala nao pa zokambirana zao zam'seri, sindifuna kukhala nao m'misonkhano yao, chifukwa choti adapha anthu mokalipa, ndipo adapundula ng'ombe zamphongo mwankhanza, naziyesa choseketsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano ao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe moyo wanga, usakhale nawo pa misonkhano yawo ya mseri, kapena kugwirizana nawo mʼmabwalo awo, pakuti anapha anthu mu mkwiyo wawo ndipo anapundula ngʼombe zamphongo monga kunawakomera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mtima wangawe, usalowe mu ciungwe cao; Ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano ao; Cifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu, M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.