Genesis 49:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Matemberero aŵagwere, chifukwa mkwiyo wao ndi woopsa kwambiri, ukali wao utembereredwenso, chifukwa imeneyo ndi nkhalwe. Ndidzaŵamwaza iwowo m'dziko lonse la Yakobe. Ndidzaŵabalalitsa pakati pa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa m'Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo m'Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi ndi ukali wawo wankhanza choterewu! Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kutembereredwekukwiyakwao, cifukwa kunali koopsya; Ndi kupsya mtima kwao, cifukwa kunali kwankharwe; Ndidzawagawanitsa m'Yakobo Ndidzabalalitsa iwo m'Israyeli.