Genesis 49:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yuda ali ngati msona wa mkango. Ukapha, umabwereranso kumalo kumene umabisala. Yuda ali ngati mkango, amatambasuka nagona pansi. Iye ndi mkangodi, ndipo palibe amene angalimbe mtima kuti amdzutse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yuda ndi mwana wa mkango, kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera; anawerama pansi, anabwatama ngati mkango, ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yuda ali ngati mwana wa mkango; umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga. Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi, ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yuda ndi mwana wa mkango, Kucokera kuzomotola, mwananga, wakwera; Anawerama pansi, anabwatama ngati mkango, Ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?