Genesis 5:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo adati, “Mwana ameneyu adzatipumuza ku ntchito zathu zolemetsazi zolima nthaka imene Chauta adaitemberera.” Ndipo mwanayo adamutcha dzina lake Nowa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
namutcha dzina lake Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa ntchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
namucha dzina lace Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa nchito zathu zobvuta za manja athu, cifukwa ca nthaka imene anaitemberera Yehova;