Genesis 50:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono nzika za ku Kanani zitaona kulira koteroko ku Atadi kuja, zidati, “Kulira kwa maliro kotereku ndi kwa ku Ejipito.” Nchifukwa chake malowo adaŵatchula kuti Abele-Miziraimu, ali kuvuma kwa Yordani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo; Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akuru a Aaigupto: cifukwa cace dzina la pamenepo linachedwa Abeli-mizraimu, pali tsidya lija la Yordano.