Genesis 50:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamwalira bambo wao uja, abale ake a Yosefe adati, “Nanga tidzatani ife, Yosefe akadzayamba kudana nafe ndi kufuna kubwezera zoipa zonse zimene tidamuchita zija?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene abale ake a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale ake a Yosefe ataona kuti abambo awo amwalira, anati, “Nanga tidzatani ngati Yosefe anatisungira mangawa nafuna kutibwezera pa zoyipa zonse zimene tinamuchitira?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene abale ace a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamcitira iye.