Genesis 50:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Ndikumpempha Yosefe kuti akhululukire cholakwa cha abale ake chimene adamchitira.’ Pepani tsopano tikhululukireni cholakwa chimene ife, akapolo a Mulungu wa atate anu, tidachita.” Atangomva zimenezi Yosefe adayambapo kulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwao, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muziti cotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kucimwa kwao, cifukwa kuti anakucitirani inu coipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa aka polo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.