Genesis 50:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakhala moyo mpaka kuwona adzukulu ake, ana a Efuremu. Pamene ana a Makiri mwana wa Manase adabadwa, Yosefe adaŵalandira m'banja mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anaona mʼbado wachitatu wa ana a Efereimu. Yosefe anatenganso ana a Makiri, mwana wa Manase kukhala ngati ana a mʼbanja lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anaona ana a Efraimu a mbadwo wacitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.