Genesis 50:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Yosefe adapempha ana a Israele kuti alumbire. Adati, “Lonjezeni kuti Mulungu akakusungani, mudzasenza mafupa anga kuchoka nawo kuno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israele kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kuchokera kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israeli lumbiro nati, “Lonjezani kuti Mulungu akadzakusungani mudzanyamula mafupa anga kuwachotsa ku malo kuno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israyeli kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kucokera kuno.