Genesis 50:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Yosefe adamwalira ali wa zaka 110. Mtembo wake adaukonza ndi mankhwala, naukhazika m'bokosi ku Ejipito komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m'bokosi m'Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lace ndi mankhwala osungira, ndipo ariamuika iye m'bokosi m'Aigupto.