Genesis 50:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ntchitoyo idaŵatengera masiku 40, monga kunkafunikira pa ntchito ya mtundu umenewo. Aejipito adalira maliro a Israele masiku 70.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatha masiku ake makumi anai a iye; chifukwa chomwecho amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aejipito anamlira iye masiku makumi asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatha masiku ace makumi anai a iye; cifukwa comweco amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aaigupto anamlira iye masiki makumi asanu ndi awiri.