Genesis 50:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapitanso ndi onse a banja lake, abale ake, ndi onse a banja la bambo wake. Ku Goseni kuja kudangotsala ana okhaokha, nkhosa zao, abusa ndi ng'ombe zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ace, ndi mbumba ya atate wace: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni.