Genesis 6:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Mulungu adauza Nowa kuti, “Ndatsimikiza mu mtima kuti ndiwononge anthu onse. Ndidzaŵaononga kotheratu chifukwa dziko lonse lapansi ladzaza ndi ntchito zao zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, “Ndatsimikiza mtima kuti ndiwononge anthu onse, pakuti dziko lapansi ladzaza ndi ntchito zawo zoyipa. Ndithudi ndiwawononga pamodzi ndi zonse za pa dziko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Cimariziro cace ca anthu onse cafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi ciwawa cifukwa ca iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.