Genesis 6:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Upange denga la chombocho, ndipo usiye mpata wa masentimita 50 pakati pa dengalo ndi mbali zake. Uchimange mosanjikiza, chikhale cha nyumba zitatu, ndipo m'mbali mwake mukhale chitseko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uike zenera m'chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m'mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uchipangire denga ndi kuchimaliza ndi zenera la masentimita makumi asanu. Uyike khomo mʼmbali mwa chombocho ndi kupanga zipinda zosanjikana; chapansi, chapakati ndi chapamwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uike zenera m'ciogalawaco, ulimarize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pace: khomo la cingalawa uike m'mbali mwace; nucipange ndi nyumba yapansi, ndi yaciwiri, ndi yacitatu.