Genesis 6:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma iweyo ndidzachita nawe chipangano. Udzaloŵe m'chombomo iwe pamodzi ndi mkazi wako, ndi ana ako pamodzi ndi akazi ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndidzachita pangano langa ndi iwe. Iwe, ana ako aamuna, mkazi wako ndi akazi a ana ako nonse mudzalowa mʼchombocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'cingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.