Genesis 6:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbalame za mtundu uliwonse ndi nyama zazikulu ndi zokwaŵa zomwe, zidzaloŵe m'chombo kuti zisungidwe ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiriziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzatenga ziwiriziwiri za mitundu yonse ya mbalame, mitundu yonse ya nyama, ndi mitundu yonse ya zokwawa kuti zikhale ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiri ziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo.