Genesis 6:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adati, “Sindidzalola anthu kukhala ndi moyo mpaka muyaya, popeza kuti munthu ndi thupi limene limafa. Kuyambira tsopano adzangokhala zaka 120.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, cifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ace adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.