Genesis 6:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku amenewo, ngakhale pambuyo pakenso, panali anthu amphamvu ataliatali pa dziko lapansi. Anthu ameneŵa ndi amene ankabadwa mwa akazi omwe adaakwatiwa ndi ana a Mulungu aja. Iwoŵa anali ngwazi zomveka ndiponso anthu otchuka pa masiku akalewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pa dziko lapansi panali anthu akulukulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masiku amenewo komanso pambuyo pake, pa dziko lapansi panali Anefili, anthu amphamvu ndiponso otchuka. Anthuwa ndi amene ankabadwa ana a Mulungu aja atakwatira ana aakazi a anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pa dziko lapansi panali anthu akurukuru masiku omwewo ndiponso pambuyo pace, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.