Genesis 6:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adati, “Anthu onse amene ndaŵalenga, ndidzaŵaononga kotheratu. Ndidzaononganso nyama zonse ndi zokwaŵa zomwe pamodzi ndi mbalame, chifukwa ndikumva chisoni kuti ndidalenga zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova anati, “Ndidzafafaniza munthu, nyama, zonse zokwawa, ndi mbalame za mu mlengalenga pa dziko lapansi, pakuti ndikumva chisoni kuti ndinazilenga zimenezi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva cisoni cifukwa ndapanga izo.