Genesis 7:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa 17, mwezi wachiŵiri, Nowa ali wa zaka 600, akasupe onse a madzi ambiri okhala pansi pa dziko adatumphuka, ndipo kuthambo kudatsekukanso, kuti madzi akhuthuke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka ca mazana asanu ndi limodzi ca moyo wa Nowa, mwezi waciwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi akuru anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.