Genesis 7:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chigumula chidagundika masiku makumi anai pa dziko lapansi. Madzi adayamba kukwera pa dziko lapansi, ndipo chombo chidayamba kuyandama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chigumula chinali pa dziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chigumula chinagwa pa dziko la pansi kwa masiku makumi anayi. Madzi anayamba kuchuluka ndipo ananyamula chombo chija ndi kuchiyandamitsa pamwamba pa dziko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cigumula cinali pa dziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anacuruka natukula cingalawa, ndipo cinakwera pamwamba pa dziko lapansi.